Malongosoledwe Amayimbidwe

Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 6

Vol.

I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

NKHOMA SYNOD

Church of Central Africa Presbyterian

VOL. I Second Edition

Golden Rules for Congregation Conductors

CONDUCTING TECHNIQUE

CCAP
(FEB, 2018)

PREPARED BY (Okonza): Eng. C. DAN Kauma

PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini
Vol. I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

MALAMULO OFUNIKA KUTSATILA POFUNA KUKWEZA


MAYIMBIDWE MUMPINGO
1. CHOLINGA CHACHIKULU CHA MAYIMBIDWE MUMPINGO
Cholinga chachikulu chakuyimba mu Mpingo ndicho kulemekeza Mulungu, ndikumuyamika
Iye. Poonjeza apo, kuyimba kumathandiza kutakasa mtima kuti anthu adzipeleke kwa
Mulungu mwakusiya zoipa zimene zimawasiyanitsa ndi Mulungu.

2. UBWINO WAKUYIMBA MUMPINGO


2.1. Oyimba amalumikizika ndi Mulungu m’kuyimba, chifukwa amazama
m’maganizo ndikumvetsetsa za Mulungu kusiyana ndi pamene palibe
kuyimba.
2.2. Oyimba amatulutsa zakukhosi kwawo kudzera mkuthamanga kwake kwa
nyimbo, kukweza kwake, liwu lake, kulumikizika kwa mawu, komanso
manvekedwe ake a nyimbo.
2.3. Kuyimba kumakongoletsa chipembedzo. Mumpingo, nyimbo zake zimapatsa
aliyense mwayi wakutula kwa Mulungu liwu lake la pamtima, lomwe
angakhale nalo. Ichi chimachitika ndi iye amene ali m’chipembedzo.

3. MAYIMBIDWE
Mayimbidwe ake a nyimbo ndi osiyanasiyana malingana ndi nyengo yake kapenanso
cholinga chake. Chitsanzo, pa nthawi ya ukwati mayimbidwe ake amakhala osiyana
ndiponso nkhope za oyimbawo zidzasiyana monga mwa nyengo yake. Maliwu anyimbo
ayenera kugwirizana ndinyengo zake. Maliwu apamaliro kapena pa ukwati kapena pa
chipembedzo aziwonetsa kusiyana pakukweza kwake. Mwa chitsanzo, pamene tikumbukira
za imfa ya Ambuye wathu Yesu Khristu. Maliwu ofanana ndi amaliro angathe kuyimbidwa.

4. WOTSOGOLERA NYIMBO PA CHIPEMBEDZO


4.4. Amawongolera onse kuti mayimbidwe amveke bwino. Ndikuti nyimbo
izithamanga moyenera monga mwachikhalidwe cha nyimbo yomwe
ikayimbidwa. Wotsogolera nyimbo ndi amene amapeleka maganizo (mood)
anyimbo kuti ikhudze kapena kusintha womvera ndiponso woyimba.
4.5. Amathandiza kuti anthu asamangokokerana kapena kulimbirana
poyambitsa nyimbo. Kapena potsogolera mizère ina m’ndime za nyimbo.
Muchizungu (Solo, Duet, Trio, Quartet ndi Choir).
4.6. Wotsogolerayo akhale wambiri yabwino. Asakhale munthu yemwe
amamveka mbiri zoyipa ku mpingo kapena kudera kumene amakhala,
kapena kumene amagwira ntchito ya muofesi kapena ya malonda. Chifukwa
PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini
Vol. I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

izi zimatsekereza kapena kuchotsa chidwi kwa anthu omvera ndi


woyimbitsidwa zimene zikaletsa kupititsa patsogole uthenga wabwino.
4.7. Akhale wodziwa bwino maliwu anyimbo ndikutsogolera kwake. Kapena kuti
akhale odziwa nyimbo zambiri komanso amene amatha kuwerenga nyimbo
muziyankhulo izi: Choyamba, Staff Notation kapena kuti zibonga, chachiwiri
ndichomaliza ndi Tonic Sol-fah kapena kuti “do do do”. Chitsanzo onani
pansi:

Figure 1. Music Scale/Ladder

4.8. Akhale wa mawu omveka bwino kapena kuti anthetemnya. Chifukwa chake
ndichakuti, anthu oyimba kawirikawiri amatengera mtsogoleri mmene
achitira. Ngati mtsogoleri ayimba mokadzula, mpingonso udzatengera
zomwezo powona ngati ndiko kuyimba koyenera
4.9. Akhale wodziwa bwino momwe nyimbo iyenera kufulumirira osati wogoneka
nyimbo kapenanso wokhadzulira poyimba ayi.
4.10. Akhale pamalo oti wonse adzimuwona.
4.11. Adzivala bwino osati mochititsa manyazi. Ngati mkutheka, avale Jaketi
komanso abophe mabatani monga chitsanzo chili m’musimu.

Figure 2. Mavalidwe Achimuna

4.12. Azikhala ndi tcheru pakuyimbitsa kuti awonetsetse kuti anthu akuyimba
mogwirizana bwino osati mokweza munthu payekha. (Balancing mu chizungu)
4.13. Ayenera kuimirira bwino pamalo owonekera
PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini
Vol. I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

4.14. Akonzekere “Key” ya nyimbo imene yatchulidwa (Zina nyimbo ndi zokwera,
zina ndi zotsika komanso zina ndi zachikatikati). Chitsanzo cha ma “Key”
anyimbo zonse zapadziko lapansi

Figure 3. Ma "Key" anyimbo

4.15. Liwiro la nyimbo (Speed) ndi kufulumira, kuchedwa ndi pakatikati (fast, slow,
ndi moderate). Izi ndi mwazina mugulu la liwiro la nyimbo (Speed). Zitsanzo
zina onani pansi:

Figure 4. Mwa mawu ena a Liwiro la nyimbo m’mchizungu

4.16. Aphunzitse anthu kuti aziwona mabiti (Beat/Conducting)


4.17. Wotsogolera aziphunzitsa nyimbo zimene siziyimbidwayimbidwa

5. MALONGOSOLEDWE APATSIKU LA MULUNGU


5.5. Woyimbitsa nyimbo pa Sabata ali ndi magawo awa:
5.5.1. Wolalikira akalonjera msonkhano, woyimbitsa nyimbo ndiye ayambe
nyimbo yoti: Yesu Mbuye Onani, Tadza poitana inu
5.5.2. Wotsogolera asayambitse ndiye “Pemphero la Ambuye”Limeneli ndigawo
la wolalikira kuyambitsa
5.5.3. Nyimbo yolemekeza iyambidwe ndi Woyambitsa nyimbo
PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini
Vol. I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

5.5.4. Wolalikira akatha kuwerenga Malamulo khumi kapena Chiphatikizo cha


malamulo khumi, ndikunena za kulapa ndi chikhululukiro, Woyimbitsa nyimbo
ndiye atsogolere nyimbo yonena zakulapa.
5.5.5. Chikhulupiliro cha chikhrisitu amene amayambitsa ndi Wolalikira osati
Woyimbitsa nyimbo ayi.
5.5.6. Woyimbitsa nyimbo ndiye amayambitsa nyimbo mpingo utatha kunena
Chikhulupiliro cha Chikhristu

1. Mayambidwe ndi matsilizidwe a nyimbo akhale bwino ndipo pomaliza nyimboyo


onse atsilizire pamodzi
2. Wotsogolera nyimbo asayambe nyimbo anthu asanadziwe kapena asanapeze
nyimboyo ayi
3. Nyimbo zoyimba pa chipembedzo zilembedwe ndikuikidwa pamalo owoneka kuti
onse azikonzekeratu. Nyimbo ziyambe zaphunzitsidwa chipembedzo chisanayambe
4. Wolalikira azilengeza nambala ya nyimbo momveka bwino kuti onse amve
ndikupezeratu
5. Wolalikirayo awerenge ndime yoyamba ndi kolasi kupereka mpata woti anthu
apeze nyimbo
6. Ngati yemwe alalikira ali ndi liwu lina la nyimboyo lomwe iye afuna kuti mpingo
uyimbe, amuuziletu wotsogolera nyimbo nthawi ya chipembedzo isanakwane
kuwopa
6. MABITI (BEATS/CONDUCTING) A NYIMBO ZIMENE TIMAYIMBA
Wotsogolera nyimbo azidziwa kuti nyimbo zili ndi mabiti ake. Afunika kutsatira mabitiwo
kuti nyimbo ziziyenda bwino. Zitsanzo za mabitiwa ndi izi:

PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini
Vol. I
Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe MAY 2018

Mabitiwa amapitilira apa (Onani zitsanzo tsamba lomaliza), zimayenera munthu


woyimbitsa nyimbo kuchita kafukufuku nthawi zonse. Chitsanzo, pakakhala maphunzilo
mumpingo kapena kwina, azitengapo mbali kuti aziwonjezera luso.

Woyimbitsa nyimbo asamavina poyimbitsa nyimbo koma asamalire za mabiti a nyimbo kuti
mpingo uyende pamodzi m’mayimbidwewo.

7. ZOWONJEZEREKA (APPENDIX)
1. Kuchita Chitsanzo (Conducting Patterns)

PREPARED BY (Okonza) Eng. C. DAN KAUMA, Mothandizidwa ndi Mr. D.E. Lubayini

You might also like